7. Ndipo musamakhala ngati makolo anu ndi abale anu, amene anai akwira Yehova Mulungu wa makolo ao, motero kuti anawapereka apasuke, monga mupenya,
8. Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m'malo ace opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wace waukali utembenuke kwa inu.
9. Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza cifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m'dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa cisomo ndi cifundo; sadzakuyang'anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye,
10. Ndipo amtokoma anapitira m'midzi m'midzi mwa dziko la Efraimu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola.
11. Komatu ena a Aseri ndi Manase ndi a Zebuloni anadzicepetsa, nadza ku Yerusalemu.
12. Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kucita cowauza mfumu ndi akuru mwa mau a Yehova.
13. Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kucita madyerero a mkate wopanda cotupitsa mwezi waciwiri, msonkhano waukuru ndithu.