2 Mbiri 30:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israyeli ndi Yuda onse, nalembanso akalata kwa Efraimu ndi Manase, kuti abwere ku nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, kucitira Yehova Mulungu wa Israyeli Paskha.

2. Pakuti mfumu idapangana ndi akuru ace, ndi msonkhano wonse wa m'Yerusalemu, kuti acite Paskha mwezi waciwiri.

3. Pakuti sanakhoza kumcita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikira, ndi anthu sadasonkhana ku Yerusalemu.

2 Mbiri 30