5. M'nyumba yaikuru tsono anacinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golidi wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo.
6. Ndipo anakuta nyumba ndi miyala ya mtengo wace; ndi golidi wace ndiye golidi wa Parivaimu.
7. Anamamatizanso kacisi, mitanda, ziundo, ndi makoma ace, ndi zitseko zace, ndi golidi; nalemba akerubi pamakoma.
8. Ndipo anamanga malo opatulikitsa, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba mikono makumi awiri, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri; naikuta ndi golidi wabwino wakufikira matalente mazana asanu ndi limodzi.
9. Ndi kulemera kwace kwa misomali ndiko masekeli makumi asanu a golidi. Ndipo anazikuta ndi golidi zipinda zosanjikizana.
10. Ndipo m'malo opatulikitsa anapanga akerubi awiri, anacita osema, nawakuta ndi golidi.
11. Ndi mapiko a akerubi m'litali mwace ndimo mikono makumi awiri; phiko la kerubi mmodzi mikono isanu, lojima khoma la nyumba; ndi phiko linzace mikono isanu, lokhudzana nalo phiko la kerubi wina.