1. Pamenepo Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wace, pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.
2. Nayamba kumanga tsiku laciwiri la mwezi waciwiri, caka cacinai ca ufumu wace.
3. Ndipo maziko adawaika Solomo akumangapo nyumba ya Mulungu ndi awa: utali wace, kuyesa mikono monga mwa muyeso wakale, ndiwo mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi kupingasa kwace mikono makumi awiri.
4. Ndi likole linali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwace monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wace zana limodzi mphambu makumr awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golidi woona.
5. M'nyumba yaikuru tsono anacinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golidi wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo.
6. Ndipo anakuta nyumba ndi miyala ya mtengo wace; ndi golidi wace ndiye golidi wa Parivaimu.