2 Mbiri 28:8-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo ana a Israyeli anatenga ndende ena a abale ao zikwi mazana awiri, akazi, ana amuna ndi akazi, nalandanso kwa iwo zofunkha zambiri, nabwera nazo zofunkhazo ku Samariya,

9. Koma panali mneneri wa Yehova pomwepo, dzina lace Odedi; naturuka iye kukomana nayo nkhondo ikudzayo ku Samariya, nanena nao, Taonani, popeza Yehova Mulungu wa makolo anu anakwiya ndi Yuda, anawapereka m'dzanja lanu, nimunawapha ndi kupsa mtima kofikira kumwamba.

10. Ndipo tsopano mukuti mugonjetse ana a Yuda ndi Yerusalemu akhale akapolo ndi adzakazi anu; palibe nanunso kodi mirandu yoparamula kwa Yehova Mulungu wanu?

11. Mundimvere tsono, bwezani andende amene munawatenga ndende a abale anu; pakuti mkwiyo waukali wa Yehova uli pa inu.

2 Mbiri 28