2 Mbiri 27:5-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Anayambananso ndi mfumu ya ana a Amoni, namgonjetsa, Ndi ana a Amoni anamninkha caka comweci matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zikwi khumi, ndi ya barele zikwi khumi. Ana a Amoni anabwera nazo zomwezo kwa iye caka caciwiri ndi cacitatu comwe.

6. Momwemo Yotamu anakula mphamvu, popeza anakonza njira zace pamaso pa Yehova Mulungu wace.

7. Macitidwe ena tsono a Yotamu, ndi nkhondo zace zonse, ndi njira zace, taonani, zalembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda.

8. Anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi mphambu zisanu ndi cimodzi.

9. Ndipo Yotamu anagona ndi makolo ace, namuika m'mudzi wa Davide; ndi Ahazi mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.

2 Mbiri 27