15. Koma Yehoyada anakalamba, nacuruka masiku, namwalira iye; ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi atatu pamene anamwalira.
16. Ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, pakati pa mafumu; pakuti anacita zabwino m'Israyeli, ndi kwa Mulungu, ndi ku nyumba yace.
17. Atamwalira Yehoyada tsono, akalonga a Yuda anadza, nalambira mfumu. Ndipo mfumu inawamvera.
18. Ndipo anasiya nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo ao, natumikira zifanizo, ndi mafano; ndipo mkwiyo unawagwera Yuda ndi Yerusalemu, cifukwa ca kuparamula kwao kumene.
19. Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawacitira umboni; koma sanawamvera.
20. Ndipo mzimu wa Mulungu unabvala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.
21. Koma anampangira ciwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova.