2 Mbiri 2:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Munditumizirenso mitengo yamikungudza, ndi yamlombwa, ndi yambawa, ya ku Lebano; pakuti ndidziwa kuti anyamata anu adziwa kutema mitengo m'Lebano; ndipo taonani, anyamata anga adzakhala ndi anyamata anu,

9. ndiko kundikonzera mitengo yambirimbiri; pakuti nyumbayi nditi ndiimange idzakhala yaikuru ndi yodabwitsa.

10. Ndipo taonani, ndidzawapatsa anyamata anu otema akulikha mitengo miyeso ya tirigu wopuntha zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya barele zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikuru ya vinyo zikwi makumi awiri, ndi mitsuko yaikufu ya mafuta zikwi makumi awiri.

11. Ndipo Huramu mfumu ya Turo anayankha ndi kulembera, natumiza kalatayo kwa Solomo, ndi kuti, Powakonda anthu ace Yehova anakulongani mfumu yao.

12. Huramu anatinso, Alemekezedwe Yehova Mulungu wa Israyeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nampatsa mfumu Davide mwana waluso, wodziwa nzeru ndi waluntha, ammangire Yehova nyumba, ndiponso nyumba ya ufumu wace.

13. Ndipo tsono ndatumiza munthu waluso wokhala Ralo, luntha, Huramu Abi,

2 Mbiri 2