1. Ndipo Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera ku nyumba yace ku Yerusalemu mumtendere.
2. Naturuka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza oipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Cifukwa ca ici ukugwerani mkwiyo wocokera kwa Yehova.