29. Ndi mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Ndidzadzizimbaitsa ndi kulowa kunkhondo, koma inu bvalani zobvala zanu. Nidzizimbaitsa mfumu ya Israyeli, namuka iwo kunkhondo.
30. Mfumu ya Aramu tsono idauza akapitao a magareta ace, ndi kuti, Musayambana ndi ang'ono kapena akuru, koma ndi mfumu ya Israyeli yekha.
31. Ndipo kunali, pamene akapitao a magareta anaona Yehosafati, anati, Ndiye mfumu ya Israyeli. Potero anamtembenukira kuyambana naye; koma Yehosafati anapfuula, namthandiza Yehova; ndipo Mulungu anawapambukitsa amleke.
32. Ndipo kunali, pamene akapitao a magareta anaona kuti sanali mfumu ya Israyeli anabwerera osamtsatanso.
33. Ndipo munthu anaponya mubvi wace ciponyeponye, namlasa pakati pa maluma a maraya ace acitsulo. Potero anati kwa woyendetsa garetayo, Tembenuza dzanja lako, nundicotse ku khamu la nkhondo kuno, pakuti ndalasidwa.
34. Ndipo nkhondo inakula tsiku lija; koma mfumu ya Israyeli inagwirizizil ka m'gareta wace popenyana ndi Aaramu mpaka madzulo, namwalira nthawi yakulowa dzuwa.