2 Mbiri 15:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo mzimu wa Mulungu unagwera Azariya mwana wa Odedi,

2. ndipo anaturuka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.

3. Masiku ambiri tsono Israyeli anakhala wopanda Mulungu woonayo, ndi wopanda wansembe wakuphunzitsa, ndi wopanda cilamulo;

4. koma pamene anatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli m'kusautsidwa kwao, ndi kumfuna, anampeza.

2 Mbiri 15