1. Ndipo kunacitika, utakhazikika ufumu wa Rehabiamu, nalimbika iye, anasiya cilamulo ca Yehova, ndi Aisrayeli onse pamodzi naye.
2. Ndipo Rehabiamu atakhala mfumu zaka zinai, Sisaki mfumu ya ku Aigupto anakwerera Yerusalemu, popeza iwo adalakwira Yehova.
3. Anakwera ndi magareta cikwi cimodzi mphambu mazana awiri, ndi apakavalo zikwi makumi asanu ndi limodzi, ndi anthu adadza naye kuturuka m'Aigupto ngosawerengeka, Alubi, Asuki, ndi Akusi.