2 Mbiri 10:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Rehabiamu anamuka ku Sekemu; pakuti Aisrayeli onse adadza ku Sekemu kumlonga ufumu.

2. Ndipo kunali, atamva Yerobiamu mwana wa Nebati (popeza anali m'Aigupto kumene adathawira, kuthawa Solomo mfumu), Yerobiamu anabwera kucoka ku Aigupto.

3. Ndipo anatuma munthu kukamuitana, nadza Yerobiamu ndi Aisrayeli onse, nalankhula ndi Rehabiamu, ndi kuti,

2 Mbiri 10