12. nzeru ndi cidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso cuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhala nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.
13. Momwemo Solomo anadza ku Yerusalemu kucokera ku msanje uli ku Gibeoni, ku khomo la cihema cokomanako; ndipo anacita ufumu pa Israyeli.
14. Ndipo Solomo anasonkhanitsa magareta ndi apakavalo, nakhala nao magareta cikwi cimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magareta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.
15. Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golidi zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza icuruke ngati mikuyu yokhala kucidikha.
16. Ndi akavalo amene Solomo anali nao anafuma ku Aigupto; amalonda a mfumu anawalandira magulu magulu, gulu liri lonse mtengo wace.