2 Mafumu 25:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali caka cacisanu ndi cinai ca ufumu wace, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babulo, iye ndi khamu lace lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.

2. Ndipo mudziwo unazingidwa ndi timalinga mpaka caka cakhumi ndi cimodzi ca mfumu Zedekiya.

2 Mafumu 25