2 Mafumu 15:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Nacita iye coipa pamaso pa Yehova, monga adacita makolo ace; sanaleka zolakwa zace za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israyeli.

10. Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamcitira ciwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwace.

11. Macitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la macitidwe a mafumu a Israyeli.

2 Mafumu 15