2 Mafumu 10:26-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Naturutsa zoimiritsa zija zinali m'nyumba ya Baala, nazitentha.

27. Nagamula fane la Baala, nagamula nyumba ya Baala, naiyesa dzala mpaka lero lino.

28. Momwemo Yehu anaononga Baala m'Israyeli.

29. Koma Yehu sanazileka zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene adacimwitsa nazo Israyeli, ndizo ana a ng'ombe agolidi okhala m'Beteli ndi m'Dani.

30. Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wacita bwino, pocita coongoka pamaso panga, ndi kucitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli.

2 Mafumu 10