2 Mafumu 10:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Nati iye, Tiye nane, ukaone cangu canga ca kwa Yehova. M'mwemo anamuyendetsa m'gareta wace.

17. Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu m'Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Elisa.

18. Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi, nanena nao, Ahabu anatumikira Baala pang'ono, koma Yehu adzamtumikira kwambiri.

19. Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ace onse, asasowe mmodzi; pakuti ndiri nayo nsembe yaikuru yocitira Baala; ali yense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Kama Yehu anacicita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.

20. Nati Yehu, Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala. Naulalikira.

2 Mafumu 10