12. Sitidzibvomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu cifukwa ca kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.
13. Pakuti ngati tiri oyaruka, titero kwa Mulungu; ngati tiri a nzeru zathu, titero kwa inu.
14. Pakuti cikondi ca Kristu citikakamiza; popeza taweruza cotero, kuti mmodzi adafera onse, cifukwa cace onse adafa;
15. ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyoasakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.