1. Cifukwa cace popeza tiri nao utumiki umene, monga talandira cifundo, sitifoka;
2. koma takaniza zobisfka za manyazi, osayendayenda mocenjerera, kapena kucita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a coonadi tidzibvomeretsa tokha ku cikumbu mtima ca anthu onse pamaso pa Mulungu.
3. Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika;
4. mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unacititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti ciwalitsiro ca Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali cithunzithunzi ca Mulungu, cisawawalire.
5. Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Kristu Yesu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, cifukwa ca Kristu.