2 Akorinto 2:15-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pakuti ife ndife pfungo labwino la Kristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena pfungo la imfa kuimfa;

16. koma kwa ena pfungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?

17. Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akucita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa coona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.

2 Akorinto 2