2 Akorinto 12:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza ku masomphenya ndi mabvumbulutso a Ambuye.

2. Ndidziwa munthu wa mwa Kristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwacitatu.

3. Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m'thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu),

4. kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.

2 Akorinto 12