1. Ndipo Samueli anamwalira; ndi Aisrayeli onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ace, namuika m'nyumba yace ku Rama. Davide nanyamuka, natsikira ku cipululu ca Parana.
2. Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wace anali ku Karimeli; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi cikwi cimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zace ku Karimeli.