1 Samueli 24:20-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israyeli udzakhazikika m'dzanja lako.

21. Cifukwa cace tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga.

22. Ndipo Davide analumbirira Sauli. Sauli namuka kwao; koma Davide ndi anthu ace anakwera kumka kungaka.

1 Samueli 24