1. Ndipo kunali, pakubwerera Sauli potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku cipululu ca Engedi.
2. Tsono Sauli anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisrayeli onse, namuka kukafuna Davide ndi anthu ace m'matanthwe a zinkhoma.
3. Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Sauli analowa kuti akapfunde mapazi ace. Ndipo Davide ndi anyamata ace analikukhala m'kati mwa phangamo,