1 Samueli 21:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Davide anafika ku Nobi kwa! Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?

2. Nati Davide kwa Ahimeleki wansembeyo, Mfumu inandilamulira nchito, ninena nane, Asadziwe munthu ali yense kanthu za nchito imene ndakutumira ndi kukulamulira; ndipo ndawapanga anyamatawo ku malo akuti.

3. Cifukwa cace tsono muli ndi ciani? mundipatse m'dzanja langa mikate isanu, kapena ciri conse muli naco.

1 Samueli 21