9. Ndipo Jonatani anati, lai ndi pang'ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukucitira coipa, sindidzadziwitsa iwe kodi?
10. Tsono Davide anati kwa Jonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa?
11. Nati Jonatani kwa Davide, Tiyeni timuke kuthengo. Namuka onse awiri kuthengoko.
12. Ndipo Jonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israyeli, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkuca, onani, pakakhala kanthu kabwino kakucitira Davide, sindidzakutumira mthenga ndi kukuululira kodi?