1 Samueli 13:1-2 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Sauli anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wace; nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.

2. Pamenepo Sauli anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israyeli; zikwi ziwiri za iwowa zinali ndi Sauli ku Mikimasi, ndi ku phiri la ku Beteli; ndi cikwi cimodzi anali ndi Jonatani ku Gibeya wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.

1 Samueli 13