8. Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israyeli anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu.
9. Ndipo anati kwa mithenga inadzayi, Muzitero kwa anthu a ku Yabezi Gileadi, Mawa litatentha dzuwa, mudzaona cipulumutso. Ndipo mithenga inadza niuza a ku Yabezi; nakondwara iwowa.
10. Cifukwa cace anthu a ku Yabezi anati, Mawa tidzaturukira kwa inu, ndipo mudzaticitira cokomera inu.