5. Ndipo m'tsogolo mwace mudzafika ku phiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumudziko mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi cisakasa, ndi lingaka, ndi toliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;
6. ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.
7. Ndipo zitakufikirani zizindikilo izi mudzacita monga mudzaona pocita, pakuti Mulungu ali nanu.
8. Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani cimene mudzacita.
9. Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samueli, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikilo zija zonse zinacitika tsiku lija.