1 Petro 5:2-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwacangu;

3. osati monga ocita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.

4. Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota. Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu.

1 Petro 5