1 Petro 5:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Kristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzabvumbulutsikawo:

2. Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwacangu;

3. osati monga ocita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.

4. Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota. Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu.

5. Koma nonsenu mubvale kudzicepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo kwa odzicepetsa.

6. Potero dzicepetseni pansi pa dzanja la mphamvu lao Mulungu, kuti panthawi yace akakukwezeni;

7. ndi kutaya pa iye nkhawa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.

1 Petro 5