1 Mbiri 9:38-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndi Mikiloti anabala Simeamu. Ndipo iwonso anakhala pamodzi ndi abale ao m'Yerusalemu, pandunji pa abale ao.

39. Ndipo Neri anabala Kisi, ndi Kisi anabala Sauli, ndi Sauli anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esbaala.

40. Ndipo mwana wa Yonatani ndiye Meribaala; ndi Meribaala anabala Mika.

1 Mbiri 9