28. Ndipo dziko lao, ndi pokhala pao ndizo Beteli ndi miraga yace, ndi kum'mawa Narani, ndi kumadzulo Gezeri ndi miraga yace, ndi Sekemu ndi miraga yace, mpaka Aza ndi miraga yace;
29. ndi kumalire a ana a Manase; Beteseani ndi miraga yace, Taanaki ndi miraga yace, Megido ndi miraga yace, Dora ndi miraga yace. M'menemo anakhala ana a Yosefe mwana wa Israyeli.
30. Ana a Aseri: Imna, ndi Isva, ndi Isvi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao.
31. Ndi ana a Beriya: Heberi, ndi Malikieli, ndiye atate wa Birizaiti.
32. Ndi Heberi anabala Yafteti, ndi Someri, ndi Hotamu, ndi Suwa mlongo wao.
33. Ndi ana a Yafteti: Pasaki, ndi Bimali, ndi Asvati. Awa ndi ana a Yafteti.
34. Ndi ana a Semeri: Ahi, ndi Roga, Yehuba, ndi Aramu.
35. Ndi ana a Helemu mbale wace: Zofa, ndi Imna, ndi Selesi, ndi Amali.
36. Ana a Zofa: Suwa, ndi Harineferi, ndi Sauli, ndi Beri, ndi Imra,
37. Bezeri, ndi Hndi, ndi Sama, ndi Silisa, ndi Itirani, ndi Beera.
38. Ndi ana a Yeteri: Yefune, ndi Pisipa, ndi Ara.