1 Mbiri 7:20-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndi ana a Efraimu: Sutera, ndi Beredi mwana wace, ndi Tahati mwana wace, ndi Ekada mwana wace, ndi Tahati mwana wace,

21. ndi Zabadi mwana wace, ndi Sutela mwana wace, ndi Ezeri, ndi Eleadi, amene anthu a Gadi obadwa m'dziko anamupha, popeza anatsikira kukalanda zoweta zao.

22. Ndipo Efraimu atate wao, anacita maliro masiku ambiri, ndi abale ace anadza kudzamtonthoza mtima.

23. Ndipo analowa kwa mkazi wace, naima iye, nabala mwana, namucha dzina lace Beriya, popeza m'nyumba mwace mudaipa.

24. Ndipo mwana wace wamkazi ndiye Seera, amene anamanga Beti-horoni wa kunsi, ndi Beti-horoni wa kumtunda, ndi Uzeniseera.

25. Ndipo Refa anali mwana wace, ndi Resefe, ndi Tela mwana wace, ndi Tahani mwana wace,

26. Ladana mwana wace, Amihudi mwana wace, Elisamu mwana wace,

27. Nuni mwana wace, Yoswa mwana wace.

28. Ndipo dziko lao, ndi pokhala pao ndizo Beteli ndi miraga yace, ndi kum'mawa Narani, ndi kumadzulo Gezeri ndi miraga yace, ndi Sekemu ndi miraga yace, mpaka Aza ndi miraga yace;

1 Mbiri 7