1. Ana a Isakara ndiwo Tola, ndi Pua, Yasubu ndi Simironi; anai.
2. Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Repaya, ndi Yerieli, ndi Yamai, ndi Ibsamu, ndi Semueli, akuru a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.
3. Ndi mwana wa Uzi: Izrahiya; ndi ana a Izrahiya: Mikaeli, ndi Obadiya, ndi Yoeli, ndi Isiya; onse asanuwa ndiwo akuru.
4. Ndi pamodzi nao mwa mibadwo yao, mwa nyumba za makolo ao, panali magulu a nkhondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi, popeza anacuruka akazi ao ndi ana ao.
5. Ndi abale ao mwa mabanja onse a Isakara, ngwazi zamphamvu, oyesedwa mwa cibadwidwe cao, onsewa ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu zisanu ndi ziwiri.
6. Ana a Benjamini ndiwo Bela, ndi Bekeri, ndi Yedyaeli, atatu.
7. Ndi ana a Bela: Ezboni, ndi Uzi, ndi Uzieli, ndi Yerimoti, ndi hi, asanu; akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zamphamvu, owerengedwa m'mabuku a cibadwidwe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza makumi atatu ndi anai.
8. Ndi ana a Bekeri: Zemira, ndi Yoasi, ndi Eliezeri, ndi Eliunai, ndi Omri, ndi Yeremoti, ndi Abiya, ndi Anatoti, ndi Alemeti. Onsewa ndiwo ana a Bekeri.