1 Mbiri 4:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ana a Yuda: Perezi, Hezroni, ndi Karmi, ndi Huri, ndi Sobala.

2. Ndipo Reaya mwana wa Sobala anabala Yahati; ndi Yahati anabala Ahumai, ndi Lahadi. Iwo ndiwo mabanja a Azorati.

3. Iwo ndiwo a atate wa Etamu: Yezreeli, ndi Isma, ndi Idibasi; ndipo dzina la mlongo wao ndiye Hazeleleponi,

4. ndi Penueli atate wa Gedoro, ndi Ezeri atate wa Husa. Awa ndi ana a Huri woyamba wa Efrata atate wa Betelehemu.

5. Ndipo Asuri atate wa Tekowa anali nao akazi awiri: Hela, ndi Naara.

6. Ndi Naara anambalira Ahuzamu, ndi Heferi, ndi Temeni, ndi Hahastario Iwo ndiwo ana a Naara.

7. Ndi ana a Hela ndiwo Zereti, lzara, ndi Etinani.

8. Ndipo Hakozi anabala Anubu, ndi Zobeba, ndi mabanja a Ahareli mwana wa Harumu.

9. Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ace; ndi mace anamucha dzina lace Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu.

10. Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israyeli, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti coipa cisandibvute. Ndipo Mulungu anafikitsa copempha iye.

11. Ndipo Kelubu mbale wa Sua anabala Mehiri, ndiye atate wa Esitoni.

12. Ndi Esitoni anabala Betirafa, ndi Paseya, ndi Tehina atate wa Irinahasi. Awa ndi anthu a Reka.

1 Mbiri 4