1 Mbiri 26:31-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Yeriya ndiye mkuru wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Caka ca makumi anai ca ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazeri wa ku Gileadi.

32. Ndi abale ace ngwazi ndiwo zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri, akuru a nyumba za makolo, amene mfumu Davide anaika akhale oyang'anira a Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, pa zinthu zonse za Mulungu ndi zinthu za mfumu.

1 Mbiri 26