Yeriya ndiye mkuru wa Ahebroni, wa Ahebroni monga mwa mibadwo ya nyumba za makolo. Caka ca makumi anai ca ufumu wa Davide anafunafuna, napeza mwa iwowa ngwazi zamphamvu ku Yazeri wa ku Gileadi.