18. Ana a Izara: wamkuru ndiye Selomiti.
19. Ana a Hebroni: wamkuru ndi Yeriya, waciwiri ndi Amariya, wacitatu ndi Yehazieli, wacinai ndi Yekameamu,
20. Ana a Uzieli: wamkuru ndi Mika, waciwiri ndi Isiya.
21. Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi ana a Mali: Eleazara ndi Kisi.
22. Nafa Eleazara wopanda ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndi asuweni ao ana a Kisi anawatenga akhale akazi ao.
23. Ana a Musi: Mali, ndi Ederi, ndi Yeremoti; atatu.
24. Awa ndi ana a Levi monga mwa nyumba za makolo ao, ndiwo akuru a nyumba za makolo a iwo owerengedwa mwa ciwerengo ca maina mmodzi mmodzi, akugwira nchito ya utumiki wa nyumba ya Yehova, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu.
25. Pakuti Davide anati, Yehova Mulungu wa Israyeli wapumulitsa anthu ace; ndipo akhala m'Yerusalemu kosatha;
26. ndiponso Alevi asasenzenso kacisi ndi zipangizo zace zonse za utumiki wace.