1 Mbiri 19:7-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Momwemo anadzilembera magareta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ace; nadza iwo, namanga misasa cakuno ca Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.

8. Pamene Davide anamva ici anatuma Yoabu ndi gulu lonse la anthu amphamvu.

9. Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo ku cipata ca mudzi, ndi mafumu adadzawo anali pa okha kuthengo.

10. Pakuona Yoabu tsono kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, anasankha amuna osankhika onse a Israyeli, nawanika ayambane ndi Aaramu.

11. Ndipo anthu otsala anawapereka m'dzanja la Abisai mbale wace; ndipo anadzinika avambane ndi ana a Amoni.

12. Ndipo anati, Akandilaka Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakulaka ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.

13. Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi midzi ya Mulungu wathu; ndipo Yehova acite comkomera.

14. Pamenepo Yoabu ndi anthu anali naye anayandikira pamaso pa Aaramu kulimbana nao, ndipo anawathawa.

15. Ndipo pakuona ana a Amoni kuti adathawa Aaramu, iwo omwe anathawa pamaso pa Abisai mbale wace, nalowa m'mudzi. Pamenepo Yoabu anadza ku Yerusalemu.

1 Mbiri 19