1 Mbiri 17:25-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Pakuti Inu, Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzammangira banja; momwemo mtumiki wanu waona mtima wakupemphera pamaso panu.

26. Ndipo tsopano, Yehova, Inu ndinu Mulungu, ndipo mwanenera mtumiki wanu cokoma ici;

27. cakukomerani kudalitsa nyumba ya mtumiki wanu, kuti ikhalebe kosatha pamaso panu; pakuti Inu Yehova mwadalitsa, ndipo idzadalitsika kosatha.

1 Mbiri 17