1. Ndipo pokhala Davide m'nyumba mwace, Davideyo anati kwa Natani mneneri, Taona, ndikhala ine m'nyumba yamikungudza, koma Gkasa la cipangano likhala m'nsaru zocinga.
2. Ndipo Natani anati kwa Davide, Mucite zonse ziri m'mtima mwanu; pakuti Mulungu ali nanu.
3. Ndipo usiku womwewo mau a Mulungu anadzera Natani, ndi kuti,
4. Kauze Davide mtumiki wanga, Atero Yehova, Usandimangire nyumba yokhalamo;