1 Mbiri 15:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Momwemo ansembe ndi Alevi anadzipatula kuti akwere nalo likasa la Yehova Mulungu wa Israyeli.

15. Ndipo ana a Alevi anasenza likasa la Mulungu pa mapewa ao, mphiko ziri m'mwemo, monga Mose anawauza, monga mwa mau a Yehova.

16. Ndipo Davide ananena ndi mkuru wa Alevi kuti aike abale ao oyimbawo ndi zoyimbira, zisakasa, ndi azeze, ndi nsanje, azimveketse ndi kukweza mau ao ndi cimwemwe.

17. Ndipo Alevi anaika Hemani mwana wa Yoeli, ndi a abale ace Asafu mwana wa Berekiya, ndi a ana a Merari, abale ao, Etani mwana wa Kusaya;

18. ndi pamodzi nao abale ao a kulongosola kwaciwiri, Zekariya, Beni, ndi Yaazieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Uni, Bliabu, ndi Benaya, ndi Maaseya, ndi Matitiya, ndi Blifelehu, ndi Mikineya, ndi Obedi Bdomu, ndi Yeieli, ndikirawo.

19. Oyimba tsono: Hemani, Asafu, ndi Btani, anayimba ndi nsanje zamkuwa;

20. ndi Zekariya, ndi Azieli, ndi Semiramod, ndi Yehieli, ndi Uni, ndi Bliabu, ndi Maaseya, ndi Benaya, ndi zisakasa kuyimbira mwa Alimoti;

21. ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikeya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi Azaziya, ndi azeze akuyimbira mwa Seminiti, kutsogolera mayimbidwe.

22. Ndi Kenaniya mkuru wa Alevi anayang'anira kusenzako; anawalangiza za kusenza, pakuti anali waluso.

23. Ndi Berekiya ndi Elikana anali odikira likasa.

24. Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netaneli, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obedi Edomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.

1 Mbiri 15