1 Mbiri 13:9-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo pamene anafika ku dwale la Kidoni, Uza anatambasula dzanja lace kulicirikiza likasa, pakuti ng'ombe zikadapulumuka.

10. Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, cifukwa anatambasulira likasa dzanja lace, nafa komweko pamaso pa Mulungu.

11. Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adacita cipasulo ndi Uza; motero anacha malowo Perezi Uza, mpaka lero lino.

1 Mbiri 13