34. Ndi a Nafitali atsogoleri cikwi cimodzi, ndi pamodzi nao ogwira zikopa ndi mikondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri.
35. Ndi a Adani akupangira nkhondo zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi zitatu kudza mazana asanu ndi limodzi.
36. Ndi a Aseri akuturuka kukhamu, akupangira nkhondo, zikwi makumi anai.
37. Ndi tsidya lga la Yordano a Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la: Manase logawika pakati, ndi zida: ziri zonse za khamu kucita nazo nkhondo, zikwi zana limodzi ndi makumi awiri.
38. Onsewa, ndiwo anthu a nkhondo akusunga malongosoledwe a nkhondo, anadza ku Hebroni ndi mtima wangwiro kudzamlonga Davide mfumu ya Aisraeli onse; ndi onse otsala a Israyeli omwe anali a mtima umodzi kumlonga Davide ufumu.