1 Mbiri 11:24-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Izi anazicita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo.

25. Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafikana atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkuru wa olindirira ace.

26. Ndipo amphamvuwo a magulu a nkhondo ndiwo Asaheli mbale wa Yoabu, Elanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

27. Samoti Mharori, Helezi Mpeloni,

28. Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekoi, Abiezeri wa ku Anatoti,

29. Sibekai Mhusati, liai M-ahohi,

30. Maharai Mnetofati, Heledi mwana wa Bana Mnetofati,

31. Itai mwana wa Ribai wa Gibeya wa ana a Benjamini, Benaya Mpiratoni,

32. Horai wa ku mitsinje ya Gaasi, Abiyeli M-ariba,

33. Azmaveti Mbaharumi, Eliaba Mshaliboni;

34. ana a Hasemu Mgizoni; Yonatani mwana wa Sage Mharari,

1 Mbiri 11