44. Ndipo anafa Bela; ndi Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozra anakhala mfumu m'malo mwace.
45. Namwalira Yobabi; ndi Husamu wa ku dziko la Atemani anakhala mfumu m'malo mwace.
46. Namwalira Husamu; ndi Hadada mwana wa Bedadi, amene anakantha Midyani ku thengo la Moabu, anakhala mfumu m'malo mwace; ndi dzina la mudzi wace ndi Aviti.
47. Namwalira Hadada; ndi Samla wa ku Masereka anakhala mfumu m'malo mwace.