1. Ndipo mfumu Solomo anali mfumu ya Israyeli yense.
2. Ndipo akuru a mfumu ndi awa: Azariya mwana wa Zadoki anali nduna,
3. Elihorepa ndi Ahiya ana a Sisa alembi, Yehosafati mwana wa Ahiludi wolembera mbiri,
4. ndi Benaya mwana wa Yehoyada anali kazembe wa nkhondo, ndi Zadoki ndi Abyatara anali ansembe,