5. Momwemo iye anamuka, nacita monga mwa mau a Yehova, nakakhala kumtsinje Keriti uli ku Yordano.
6. Ndipo makungubwi anamtengera mkate ndi nyama m'mawa, ndi mkate ndi nyama madzulo; namamwa iye mumtsinje.
7. Ndipo kunacitika, atapita masiku ena mtsinje udaphwa, popeza munalibe mvula m'dziko.
8. Ndipo mau a Yehova anadza kwa iye, nati,
9. Nyamuka, pita ku Zarefati wa ku Zidoni, nukhale kumeneko; taona, ndamlamulira mkazi wamasiye wa kumeneko akudyetse.
10. Tsono iye ananyamuka namka ku Zarefati, nafika ku cipata ca mudzi; ndipo taona mkazi wamasiye anali kutola nkhuni; ndipo iye anamuitana, nati, Unditengere madzi pang'ono m'cikho, ndimwe.